Jeremiah 44:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Mwaziwona zoopsa zimene ndidagwetsa pa Yerusalemu ndi mizinda yonse ya ku Yuda. Tsopano yonseyo yasanduka mabwinja, yopanda anthu okhalamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Mwaona choipa chonse chimene ndatengera pa Yerusalemu, ndi pa midzi yonse ya Yuda; ndipo, taonani, lero lomwe ili bwinja, palibe munthu wokhalamo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Inu mwaona mavuto aakulu amene ndinawabweretsa pa Yerusalemu ndi mizinda yonse ya Yuda. Lero mizinda yonseyo yasanduka mabwinja, yopanda munthu wokhalamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Mwaona coipa conse cimene ndatengera pa Yerusalemu, ndi pa midzi yonse ya Yuda; ndipo, taonani, lero lomwe iri bwinja, palibe munthu wokhalamo;