Jeremiah 44:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Za lubani amene munkafukiza inuyo, makolo anu, mafumu anu, akalonga anu ndi anthu am'dzikomo, m'mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya mu Yerusalemu, kodi muyesa kuti Chauta adaziiŵala? Kodi nkupanda kuzikumbukira mumtima mwake?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zofukizira zanu m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, za inu ndi atate anu, mafumu anu ndi akulu anu, ndi anthu a m'dziko, kodi Yehova sanazikumbukire, kodi sizinalowe m'mtima mwake?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi mukuganiza kuti Yehova nʼkuyiwala kuti inuyo ndi makolo anu, mafumu anu ndi akuluakulu anu, ndiponso anthu onse, munkafukiza lubani kwa mafano a mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zofukizira zanu m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, za inu ndi atate anu, mafumu anu ndi akuru anu, ndi anthu a m'dziko, kodi Yehova sanazikumbukira, kodi sizinalowa m'mtima mwace?