Jeremiah 44:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Chauta sadathenso kupirira ntchito zanu zoipa ndi zonyansa zimene munkachita. Choncho dziko lanu lidasanduka chipululu, chinthu choopsa ndi chotembereredwa, dziko lopanda anthu, monga liliri leromu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova sanathe kupirirabe, chifukwa cha machitidwe anu oipa, ndi chifukwa cha zonyansa zimene munazichita; chifukwa chake dziko lanu likhala bwinja, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiye Yehova sakanathanso kupirira ndi machitidwe anu ndi zonyansa zimene munkachita. Nʼchifukwa chake dziko lanu linasanduka chipululu, chinthu choopsa ndi chotembereredwa. Dziko lopandamo anthu monga zilili lero lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo Yehova sanatha kupirirabe, cifukwa ca macitidwe anu oipa, ndi cifukwa ca zonyansa zimene munazicita; cifukwa cace dziko lanu likhala bwinja, ndi cizizwitso, ndi citemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe.