Jeremiah 44:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsoka limeneli lakugwerani chifukwa choti munkafukiza lubani, ndipo munkachimwira Chauta pokana kumvera mau ake ndi posatsata malamulo ndi malangizo ake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa mwafukiza, ndi chifukwa mwachimwira Yehova, osamvera mau a Yehova, osayenda m'chilamulo chake, ndi m'malemba ake, ndi m'mboni zake, chifukwa chake choipachi chakugwerani, monga lero lomwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mavuto awa akugwerani chifukwa munkafukiza lubani ndipo munkachimwira Yehova pokana kumvera mawu ake ndi kutsatira malamulo ndi malangizo ake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa mwafukiza, ndi cifukwa mwacimwira Yehova, osamvera mau a Yehova, osayenda m'cilamulo cace, ndi m'malemba ace, ndi m'mboni zace, cifukwa cace coipaci cakugwerani, monga lero lomwe.