Jeremiah 44:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yeremiya adauzanso anthu onse, makamaka akazi, kuti, “Mverani mau a Chauta inu nonse ochokera ku Yuda amene mukukhala ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso Yeremiya anati kwa anthu onse, ndi kwa akazi onse, Tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda amene muli m'dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yeremiya anawuza anthu onse, makamaka akazi kuti, “Imvani mawu a Yehova, anthu onse a ku Yuda amene muli mu Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso Yeremiya anati kwa anthu onse, ndi kwa akazi onse, Tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda amene muli m'dziko la Aigupto.