Jeremiah 44:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, Inu ndi akazi anu mudalonjeza ndi pakamwa panupa ndipo mudazichitadi ndi manja anu. Inu mudanena kuti, ‘Tidzachita zimene talumbira. Tidzaifukizira lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuiperekera nsembe zazakumwa.’ Chabwino, tsimikizani lonjezo lanuli, ndi kuchitadi zimene mudalumbirazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Inu ndi akazi anu mwanena ndi m'kamwa mwanu, ndi kukwaniritsa ndi manja anu kuti, Tidzachita ndithu zowinda zathu taziwindira, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira; khazikitsanitu zowinda zanu, chitani zowinda zanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Inu ndi akazi anu munalonjeza ndi pakamwa panu, ndipo malonjezowo mwakwaniritsa. Inu munanena kuti, ‘Tidzachita zimene tinalonjeza, kufukizira lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuyipatsa chopereka cha zakumwa.’ Tsopano chitanitu zimene munalonjezazo! Kwaniritsani malumbiro anu. “Yambani, chitani zimene munalonjeza! Kwaniritsani malumbiro anu!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Inu ndi akazi anu mwanena ndi m'kamwa mwanu, ndi kukwaniritsa ndi manja anu kuti, Tidzacita ndithu zowinda zathu taziwindira, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira; khazikitsanitu zowinda zanu, citani zowinda zanu.