Jeremiah 44:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsono imvani mau a Chauta, inu nonse ochokera ku Yuda amene mumakhala ku Ejipito. Chauta akuti, Ndalumbira m'dzina langa lopambana kuti mwa anthu a ku Yuda palibe ndi mmodzi yemwe wodzatchulanso dzina limeneli m'dziko lino la Ejipito kuti, ‘Pali Chauta wamoyo.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda okhala m'dziko la Ejipito: Taonani, ndalumbira, Pali dzina langa lalikulu, ati Yehova, kuti dzina langa silidzatchulidwanso m'kamwa mwa munthu aliyense wa Yuda m'dziko la Ejipito, ndi kuti, Pali Yehova Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma imvani mawu a Yehova, inu Ayuda nonse amene mukukhala mu Igupto: Yehova akuti, ‘Ine ndikulumbira mʼdzina langa lopambana kuti palibe wochokera ku Yuda amene akukhala mu Igupto amene adzatchule dzina langa polumbira kuti, ‘Pali Ambuye Yehova wamoyo.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda okhala m'dziko la Aigupto: Taonani, ndalumbira, Pali dzina langa lalikuru, ati Yehova, kuti dzina langa silidzachulidwanso m'kamwa mwa munthu ali yense wa Yuda m'dziko la Aigupto, ndi kuti, Pali Yehova Mulungu.