Jeremiah 44:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panopo ndikuŵazonda kuti ndiŵachite zoipa osati zabwino. Anthu onse a ku Yuda amene ali ku Ejipito adzaphedwa pa nkhondo, ena adzafa ndi njala, mpaka nditaŵatheratu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, ndiwayang'anira kuwachitira zoipa, si zabwino; ndipo amuna onse a Yuda okhala m'dziko la Ejipito adzathedwa ndi lupanga ndi njala, mpaka kutha kwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ndionetsetsa kuti ndiwachitire choyipa, osati chabwino. Anthu a ku Yuda amene akukhala ku Igupto adzaphedwa pa nkhondo. Ena adzafa ndi njala mpaka onse atatheratu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, ndiwayang'anira kuwacitira zoipa, si zabwino; ndipo amuna onse a Yuda okhala m'dziko la Aigupto adzathedwa ndi lupanga ndi njala, mpaka kutha kwao.