Jeremiah 44:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Opulumuka ku nkhondo, amene adzabwerera ku Yuda kuchokera ku Ejipito, ndi oŵerengeka okha. Choncho otsala onse a ku Yuda amene adapita kukakhala ku Ejipito adzadziŵa kuti zoona nziti, zaozo kapena zangazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo amene adzapulumuka kulupanga adzabwera kutuluka kudziko la Ejipito kulowa m'dziko la Yuda, owerengeka; ndipo otsala onse a Yuda, amene analowa m'dziko la Ejipito kuti akhale m'menemo, adzadziwa ngati adzatsimikizidwa mau a yani, kapena anga, kapena ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amene adzapulumuke ku lupanga ndi kubwerera ku dziko la Yuda kuchokera ku Igupto adzakhala ochepa kwambiri. Choncho otsala onse a ku Yuda amene anapita kukakhala ku Igupto adzadziwa kuti mawu woona ndi ati, anga kapena awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo amene adzapulumuka kulupanga adzabwera kuturuka ku dziko la Aigupto kulowa m'dziko la Yuda, owerengeka; ndipo otsala onse a Yuda, amene analowa m'dziko la Aigupto kuti akhale m'menemo, adzadziwa ngati adzatsimikizidwa mau a yani, kapena anga, kapena ao.