Jeremiah 44:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikukupatsani chizindikiro chakuti ndidzakulangani ku malo ano, kuti choncho mudziŵe kuti mau anga oti ndidzakulangani ndi oonadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro cha kwa inu, ati Yehova, chakuti Ine ndidzakulangani m'malo muno, kuti mudziwe kuti mau anga adzatsimikizidwatu akuchitireni inu zoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine Yehova ndikukupatsani chizindikiro chakuti ndidzakulangani ku malo ano. Motero mudzadziwa kuti mawu anga akuti ndidzakulangani ndi woona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ici cidzakhala cizindikiro ca kwa inu, ati Yehova, cakuti Ine ndidzakulangani m'malo muno, kuti mudziwe kuti mau anga adzatsimikizidwatu akucitireni inu zoipa.