Jeremiah 44:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zonsezi zidachitika chifukwa cha machimo a anthu amene adaputa mkwiyo wanga, pofukizira lubani milungu ina ndi kumaitumikira, milungu imene sadaidziŵe iwowo kapena inu kapenanso makolo anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa cha choipa chao anachichita kuutsa nacho mkwiyo wanga; pakuti anapita kukafukizira, ndi kutumikira milungu ina, imene sanaidziwe, ngakhale iwo, ngakhale inu, ngakhale makolo anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimenezi zinachitika chifukwa cha zoyipa zomwe anachita. Iwo anaputa mkwiyo wanga pofukiza lubani ndi potumikira milungu ina imene iwo kapena inu ngakhalenso makolo anu sanayidziwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa ca coipa cao anacicita kuutsa naco mkwiyo wanga; pakuti anapita kukafukizira, ndi kutumikira milungu yina, Imene sanaidziwa, ngakhale iwo, ngakhale inu, ngakhale makolo anu.