Jeremiah 44:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chizindikirocho ndi ichi: Farao Hofira, mfumu ya ku Ejipito, ndidzampereka kwa adani ake, ndi kwa anthu ofuna kumupha, monga ndidamchitira Zedekiya mfumu ya ku Yuda: iyenso ndidampereka kwa mdani wake Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, amene ankafuna kumupha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova atero: Taonani, ndidzapereka Farao Hofira mfumu ya Aejipito m'manja a adani ake, ndi m'manja a iwo akufuna moyo wake; monga ndinapereka Zedekiya mfumu ya Yuda m'manja a Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni mdani wake, amene anafuna moyo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, ‘Ine ndidzamupereka Farao Hofira mfumu ya Igupto kwa adani ake amene akufuna kumupha, monga momwe ndinaperekera Zedekiya mfumu ya Yuda kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, mdani wake amene ankafuna kumupha.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova atero: Taonani, ndidzapereka Farao Hofra mfumu ya Aigupto m'manja a adani ace, ndi m'manja a iwo akufuna moyo wace; monga ndinapereka Zedekiya mfumu ya Yuda m'manja a Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo mdani wace, amene anafuna moyo wace.