Jeremiah 44:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe ine ndidakhala ndikutuma atumiki anga aneneri kuti adzakuuzeni kuti, ‘Musamachita zoipa zimene Ine ndimadana nazo.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndinatuma kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndinauka mamawa ndi kuwatuma, ndi kuti, Musachitetu chonyansa ichi ndidana nacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kawirikawiri Ine ndakhala ndikutuma atumiki anga, aneneri, amene anati, ‘Musachite chinthu chonyansachi chimene Ine ndimadana nacho!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndinatuma kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndinauka mamawa ndi kuwatuma, ndi kuti, Musacitetu conyansa ici ndidana naco.