Jeremiah 44:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero ukali wa mkwiyo wanga udayaka ngati moto m'mizinda ya ku Yuda ndi ku miseu ya mu Yerusalemu. Mizindayo idasanduka mabwinja osiyidwa, monga m'mene iliri leromu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake mkwiyo wanga ndi ukali wanga unathiridwa, nuyaka m'midzi ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu; ndipo yapasudwa nikhala bwinja, monga lero lomwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake mkwiyo wanga unayaka ngati moto kutentha mizinda ya ku Yuda ndi misewu ya mu Yerusalemu ndi kuyisandutsa bwinja mpaka lero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace mkwiyo wanga ndi ukali wanga unathiridwa, nuyaka m'midzi ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu; ndipo yapasudwa nikhala bwinja, monga lero lomwe.