Jeremiah 44:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndiye tsopano Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, Chifukwa chiyani mukuti mudziwononge chotero? Chifukwa chiyani mukufuna kuphetsa Ayuda amuna ndi akazi, ana ndi makanda, osakutsalirani ndi mmodzi yemwe pa mtundu wanu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Chifukwa chanji muchitira miyoyo yanu choipa ichi, kudzisadzira nokha amuna ndi akazi, makanda ndi oyamwa, pakati pa Yuda, osakusiyirani mmodzi yense;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndiye tsopano Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena kuti, ‘Chifukwa chiyani mukufuna kudziwononga chotere? Kodi mukufuna kuti amuna, akazi, ana ndi makanda onse aphedwe ndi kuti mu Yuda musatsale ndi munthu mmodzi yemwe?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Cifukwa canji mucitira miyoyo yanu coipa ici, kudzisadzira nokha amuna ndi akazi, makanda ndi oyamwa, pakati pa Yuda, osakusiyirani mmodzi yense;