Jeremiah 44:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chiyani mukuputa mkwiyo wanga pochita zoipa ndi manja anu ndiponso pomafukizira lubani milungu ina m'dziko la Ejipito m'mene mukukhala? Mudziwononga nokha, ndipo musanduka chinthu chomachiseka ndi chonyozeka m'maso mwa anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza muutsa mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu, pofukizira milungu ina m'dziko la Ejipito, kumene mwapita kukhalako; kuti mudulidwe, ndi kuti mukhale chitemberero ndi chitonzo mwa amitundu onse a dziko lapansi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chiyani mukuputa mkwiyo wanga popembedza mafano pofukiza lubani kwa milungu ina mʼdziko lino la Igupto mʼmene mukukhalamo. Kodi mukuchita zimenezi kuti mudziwononge nokha ndi kuti mudzisandutse chinthu choseketsa ndi chonyozeka pakati pa mitundu yonse ya dziko lapansi?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza muutsa mkwiyo wanga ndi nchito ya manja anu, pofukizira milungu yina m'dziko la Aigupto, kumene mwapita kukhalako; kuti mudulidwe, ndi kuti mukhale citemberero ndi citonzo mwa amitundu onse a dziko lapansi?