Jeremiah 45:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe Baruki udati, ‘Tsoka kwa ine, poti Chauta wandiwonjezera chisoni pa mavuto anga onse. Ndatopa nako kubuula kwanga, sindikutha kupeza mpumulo konse!’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munati, Kalanga ine tsopano! Pakuti Yehova waonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe unati, ‘Kalanga ine! Yehova wawonjezera chisoni pa mavuto anga. Ine ndatopa ndi kubuwula ndipo sindikupeza mpumulo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munati, Kalanga ine tsopano! pakuti Yehova waonjezera cisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma,