Jeremiah 45:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ukudzifunira zazikulu? Ai, usadzifunire zoterezi. Ndidzagwetsera anthu onse zoipa. Koma iwe ndidzasunga moyo wako kulikonse kumene ungapite,’ ” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi udzifunira wekha zinthu zazikulu? Usazifune; pakuti, taona, ndidzatengera zoipa pa anthu onse, ati Yehova: koma moyo wako ndidzakupatsa iwe ngati chofunkha m'malo monse m'mene mupitamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi tsono ukudzifunira wekha zinthu zazikulu? Usadzifunire. Pakuti ndidzagwetsa mavuto pa anthu onse, koma ndidzasunga moyo wako kulikonse kumene ungadzapite.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi udzifunira wekha zinthu zazikuru? usazifune; pakuti, taona, ndidzatengera zoipa pa anthu onse, ati Yehova: koma moyo wako ndidzakupatsa iwe ngati cofunkha m'malo monse m'mene mupitamo.