Jeremiah 46:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsikulo ndi tsiku la Chauta Wamphamvuzonse, tsiku lolipsira, lolipsira adani ake. Lupanga lake lidzaŵaononga, lidzakhuta magazi, lidzachita kuledzera nawo. Ambuye Chauta Wamphamvuzonse akukonzera nsembe ku dziko lakumpoto, pafupi ndi mtsinje wa Yufurate.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti tsikulo ndi la Ambuye, Yehova wa makamu, tsiku lakubweza chilango, kuti abwezere chilango adani ake; ndipo lupanga lidzadya, lidzakhuta, nilidzamwetsa mwazi wao; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi nsembe m'dziko la kumpoto pa mtsinje wa Yufurate.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tsikulo ndi la Ambuye Yehova Wamphamvuzonse; tsiku lolipsira, lolipsira adani ake. Lupanga lake lidzawononga ndi kukhuta magazi, lidzaledzera ndi magazi. Pakuti Yehova, Yehova Wamphamvuzonse, adzapereka adani ake ngati nsembe mʼdziko la kumpoto mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti tsikulo ndi la Ambuye, Yehova wa makamu, tsiku lakubweza cilango, kuti abwezere cilango adani ace; ndipo lupanga lidzadya, lidzakhuta, nilidzamwetsa mwazi wao; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi nsembe m'dziko la kumpoto pa nyanja ya Firate.