Jeremiah 46:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mulengeze ku Ejipito, mulalike ku Migidoli, ku Memfisi ndi ku Tapanesi. Anthu akumeneko muŵauze kuti, ‘Imani pamalo panu, mukhale okonzeka chifukwa chakuti nkhondo idzaononga zonse pokuzungulirani.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nenani m'Ejipito, lalikirani m'Migidoli, lalikirani m'Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mulengeze ku Igupto. Mulengeze ku Migidoli. Mulengezenso ku Mefisi ndi ku Tapanesi. Muwawuze anthu akumeneko kuti, ‘Imani pamalo panu ndi kukhala okonzeka kudziteteza, chifukwa lupanga lidzawononga zonse zimene muli nazo.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nenani m'Aigupto, lalikirani m'Migidoli, lalikirani m'Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako.