Jeremiah 46:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ako akukhumudwa, akugwerana. Aliyense akunena kuti, ‘Nyamukani, tiyeni tizibwerera kwathu, kudziko kumene tidabadwira, tithaŵe lupanga la adani athuŵa!’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anaphunthwitsa ambiri, inde, anagwa wina pa mnzake, ndipo anati, Ukani, tinkenso kwa anthu athu, kudziko la kubadwa kwathu, kuchokera kulupanga lovutitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ankhondo anu apunthwa ndi kugwa. Aliyense akuwuza mnzake kuti, ‘Tiyeni tibwerere kwathu, ku dziko kumene tinabadwira, tithawe lupanga la adani athu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anapunthwitsa ambiri, inde, anagwa wina pa mnzace, ndipo anati, Ukani, tinkenso kwa anthu athu, ku dziko la kubadwa kwathu, kucokera ku lupanga lobvutitsa.