Jeremiah 46:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pali Ine ndemwe!” Ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse. Wina wamphamvu adzabwera wonga ngati Tabori phiri lopambana mapiri ena, wonga ngati phiri la Karimele, loti joo m'mbali mwa nyanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pali Ine, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu, ndithu monga Tabori mwa mapiri, monga Karimele pambali pa nyanja, momwemo adzafika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pali Ine wamoyo,” ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse, “wina adzabwera amene ali ngati Tabori phiri lopambana mapiri ena, ngati phiri la Karimeli loti njoo mʼmbali mwa nyanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pali Ine, ati Mfumu, dzina lace ndi Yehova wa makamu, ndithu monga Tabori mwa mapiri, monga Karimeli pambali pa nyanja, momwemo adzafika.