Jeremiah 46:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunena za Ejipito, adanena za gulu lankhondo la Farao Neko, mfumu ya ku Ejipito, limene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adaligonjetsa ku Karikemisi ku mtsinje wa Yufurate pa chaka chachinai cha ufumu wa Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda. Adati,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Za Ejipito: kunena za nkhondo ya Farao Neko mfumu ya Aejipito, imene inali pa mtsinje wa Yufurate m'Karikemisi, imene anaikantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kunena za Igupto: Yehova ananena za gulu lankhondo la Farao Neko mfumu ya ku Igupto limene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni analigonjetsa ku Karikemesi ku mtsinje wa Yufurate mʼchaka cha chinayi cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Za Aigupto: kunena za nkhondo ya Farao-neko mfumu ya Aigupto, imene inali pa nyanja ya Firate m'Karikemisi, imene anaikantha Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo caka cacinai ca Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda.