Jeremiah 46:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankhondo aganyu amene ali nawo, ali ngati anaang'ombe onenepa. Nawonso abwerera m'mbuyo nathaŵa pamodzi, palibe amene walimbikira. Ndithu, nthaŵi ya tsoka yaŵafikira, ndiyo nthaŵi yoŵalanga!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso olipidwa ake ali pakati pake onga ngati anaang'ombe a m'khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale ankhondo aganyu amene ali naye ali ngati ana angʼombe onenepa. Nawonso abwerera mʼmbuyo, nathawa pamodzi. Palibe amene wachirimika. Ndithu, tsiku la tsoka lawafikira; ndiyo nthawi yowalanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso olipidwa ace ali pakati pace onga ngati ana a ng'ombe a m'khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao.