Jeremiah 46:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Liwu la Ejipito likunga ngati la njoka yothaŵa, chifukwa choti adani ake abwera ndi zida zao, kubwera ndi nkhwangwa, ngati anthu odula mitengo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mkokomo wake udzanga wa njoka yothawa; pakuti adzayenda ndi nkhondo, adzafika kumenyana naye ndi nkhwangwa, monga akutema mitengo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aigupto akuthawa ndi liwu lawo lili ngati la njoka yothawa pamene adani abwera ndi zida zawo, abwera ndi nkhwangwa ngati anthu odula mitengo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mkokomo wace udzanga wa njoka yothawa; pakuti adzayenda ndi nkhondo, adzafika kumenyana naye ndi nkhwangwa, monga akutema mitengo.