Jeremiah 46:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, wanena kuti, “Ndidzalanga Amoni, mulungu wa Thebesi. Ndidzalanganso Farao ndi Ejipito pamodzi ndi milungu yake ndi akalonga ake. Ndidzalanga Farao ndi onse amene amamkhulupirira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, ati: Taonani, ndidzalanga Amoni wa No, ndi Farao, ndi Ejipito, pamodzi ndi milungu yake, ndi mafumu ake; ngakhale Farao, ndi iwo akumkhulupirira iye;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena kuti, “Ndili pafupi kulanga Amoni mulungu wa Tebesi. Ndidzalanganso Farao ndi Igupto pamodzi ndi milungu yake yonse, mafumu ake ndi onse amene amamukhulupirira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, ati: Taonani, ndidzalanga Amoni wa No, ndi Farao, ndi Aigupto, pamodzi ndi milungu yace, ndi mafumu ace; ngakhale Farao, ndi iwo akumkhulupirira iye;