Jeremiah 46:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaŵapereka kwa amene afuna kuŵaononga, ndiye kuti kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, ndi atsogoleri ake a ankhondo. Komabe patapita nthaŵi, Ejipito adzakhalanso ndi anthu monga kale,” akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndidzawapereka m'manja a iwo amene afuna moyo wao, ndi m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'manja a atumiki ake; pambuyo pake adzakhalamo anthu, monga masiku akale, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawapereka kwa amene akufuna kuwapha, ndiye kuti kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi atsogoleri ake ankhondo. Komabe, mʼtsogolomo Igupto adzakhalanso ndi anthu monga kale,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndidzawapereka m'manja a iwo amene afuna moyo wao, ndi m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, ndi m'manja a atumiki ace; pambuyo pace adzakhalamo anthu, monga masiku akale, ati Yehova.