Jeremiah 46:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma iwe Yakobe, mtumiki wanga, usachite mantha, Iwe Israele, usataye mtima, chifukwa ndidzakupulumutsa kuchokera ku maiko akutali. Ndidzapulumutsanso zidzukulu zako kuchokera kumaiko kumene adapita nazo ku ukapolo. Yakobe adzabwerera, nadzapumula pabwino, ndi pa mtendere. Palibe winanso amene adzamuwopsa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma usaope iwe, mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha, iwe Israele: pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kuchokera kutali, ndi mbeu yako kudziko la undende wao, ndipo Yakobo adzabwera, nadzapumula m'mtendere, ndipo palibe amene adzamuopetsa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha; usataye mtima, iwe Israeli. Ndithu Ine ndidzakupulumutsa kuchokera ku mayiko akutali, ndidzapulumutsanso zidzukulu zako kuchokera ku mayiko kumene anapita nazo ku ukapolo. Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala motakasuka ndi pa mtendere, ndipo palibenso wina amene adzamuopsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma usaope iwe, mtumiki wanga Yakobo, usacite mantha, iwe Israyeli: pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kucokera kutari, ndi mbeu yako ku dziko la undende wao, ndipo Yakobo adzabwera, nadzapumula m'mtendere, ndipo palibe amene adzamuopetsa iye,