Jeremiah 46:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Iwe Yakobe, mtumiki wanga, usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe. Ndidzaonongeratu mitundu yonse ya anthu a kumaiko kumene ndidakupirikitsira. Koma iweyo sindidzakuwononga kotheratu ai. Kulanga ndidzakulanga monga m'mene kuyenera, sindingakulekelere osakulanga konse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; pakuti Ine ndili ndi iwe; pakuti Ine ndidzathetsa mitundu yonse kumene ndinakuingitsirako iwe, koma sindidzakuthetsa iwe; koma ndidzakulangiza ndi chiweruziro, ndipo sindidzakusiya konse wosalangidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe,” akutero Yehova. “Ndidzawonongeratu mitundu yonse ya anthu a ku mayiko kumene ndakupirikitsira, Koma iwe sindidzakuwononga kotheratu. Ndidzakulanga iwe ndithu koma moyenerera; sindidzakulekerera osakulanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; pakuti Ine ndiri ndi iwe; pakuti Ine ndidzathetsa mitundu yonse kumene ndinakuingitsirako iwe, koma sindidzakuthetsa iwe; koma ndidzakulangiza ndi ciweruziro, ndipo sindidzakusiya konse wosalangidwa.