Jeremiah 46:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsopano ndikuwona chiyani? Achita mantha, abwerera. Ankhondo ao agonjetsedwa. Akuthaŵa kaŵeraŵera, osacheukanso m'mbuyo. Agwidwa ndi mantha ponseponse,” akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chanji ndachiona? Aopa, abwerera; amphamvu ao agwetsedwa, athawadi, osacheukira m'mbuyo; mantha ali ponseponse, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yeremiya anati: Kodi ndikuona chiyani? Achita mantha akubwerera, ankhondo awo agonjetsedwa. Akuthawa mofulumirapo osayangʼananso mʼmbuyo, ndipo agwidwa ndi mantha ponseponse,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa canji ndaciona? aopa, abwerera; amphamvu ao agwetsedwa, athawadi, osaceukira m'mbuyo; mantha ali ponseponse, ati Yehova.