Jeremiah 46:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ejipito akukwera ngati mtsinje wa Nailo, ngati mitsinje ya madzi achigumula. Akuti, ‘Ndidzambatuka ndi kuliphimba dziko lapansi. Ndiwononga mizinda ndi anthu ake.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ejipito auka ngati Nailo, madzi ake agavira ngati nyanja; ndipo ati, Ndidzauka, ndidzamiza dziko lapansi; ndidzaononga mudzi ndi okhalamo ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Igupto akusefukira ngati Nailo, ngati mitsinje ya madzi amkokomo. Iye akunena kuti, ‘Ndidzadzuka ndi kuphimba dziko lapansi; ndidzawononga mizinda ndi anthu ake.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Aigupto auka ngati Nile, madzi ace agabvira ngati nyanja; ndipo ati, Ndidzauka, ndidzamiza dziko lapansi; ndidzaononga mudzi ndi okhalamo ace.