Jeremiah 46:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tiyeni inu akavalo, thamangani inu magaleta. Pitani patsogolo inu ankhondo, inu anthu a ku Etiopiya ndi a ku Puti, ogwira zishango, ndiponso inu anthu a ku Ludi, akatswiri pogwira uta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwerani, inu akavalo; chitani misala, inu magaleta, atuluke amphamvu; Akusi ndi Aputi, ogwira chikopa; ndi Aludi, amene agwira ndi kukoka uta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tiyeni, inu akavalo! Thamangani inu magaleta! Tulukani, inu ankhondo, ankhondo a ku Kusi ndi Puti amene mumanyamula zishango, ankhondo a ku Ludi amene mumaponya uta.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwerani, inu akavalo; citani misala, inu magareta, aturuke amphamvu; Akusi ndi Aputi, ogwira cikopa; ndi Aludi, amene agwira ndi kukoka uta.