Jeremiah 47:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adati, “Onani m'mene madzi akubwerera kuchokera kumpoto, adzakhala mtsinje wosefukira ndi wamkokomo. Adzasefukira m'dzikomo ndi kumiza zonse zokhala m'menemo, mizinda yonse, ndi anthu onse okhalamo. Anthu azidzafuula, onse okhala m'dzikomo azidzalira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova atero: Taonani, madzi adzakwera kutuluka kumpoto, nadzakhala mtsinje wosefuka, nadzasefukira padziko ndi pa zonse zili m'mwemo, pamudzi ndi pa onse okhalamo; ndipo amuna adzalira, ndi onse okhala m'dziko adzakuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Taonani mmene madzi akubwerera kuchokera kumpoto; adzasanduka mtsinje wosefukira ndi a mkokomo. Adzasefukira mʼdziko monse ndi kumiza chilichonse mʼmenemo, mizinda ndi onse okhala mʼmenemo. Anthu adzafuwula; anthu onse okhala mʼdzikomo adzalira
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova atero: Taonani, madzi adzakwera kuturuka kumpoto, nadzakhala mtsinje wosefuka, nadzasefukira padziko ndi pa zonse ziri m'mwemo, pamudzi ndi pa onse okhalamo; ndipo amuna adzalira, ndi onse okhala m'dziko adzakuwa.