Jeremiah 47:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
A ku Gaza adzameta mipala yachisoni, A ku Asikeloni adzangoti chete. Inu otsala mwa Afilisti, kodi ndi mpaka liti mudzakhale mukudzichekacheka chifukwa cha kulira?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dazi lafikira a Gaza; Asikeloni wathedwa, otsala m'chidikha chao; udzadzicheka masiku angati?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Gaza ameta mipala; anthu a ku Asikeloni akhala chete. Inu otsala a ku chigwa, mudzakhala mukudzichekacheka mpaka liti?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dazi lafikira a Gaza; Asikeloni wathedwa, otsala m'cidikha cao; udzadziceka masiku angati?