Jeremiah 48:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ponena za Mowabu, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, “Tsoka kwa mzinda wa Nebo, wasanduka chipululu. Kiriyataimu wachititsidwa manyazi, wagonjetsedwa. Linga lake lankhondo alinyoza ndipo aligumula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Za Mowabu. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Tsoka Nebo! Pakuti wapasuka; Kiriyataimu wachitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lachitidwa manyazi lapasudwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ponena za Mowabu: Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Tsoka kwa mzinda wa Nebo, chifukwa wawonongedwa. Mzinda wa Kiriyataimu wachititsidwa manyazi ndipo wagonjetsedwa; linga lichititsidwa manyazi ndipo lagumulidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Za Moabu Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Tsoka Nebo! pakuti wapasuka; Kiriyataimu wacitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lacitidwa manyazi lapasudwa.