Jeremiah 48:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira unyamata wake, ngati vinyo wokhazikika pa masese ake, osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina kuthira mu mtsuko wina. Sadatengedwe ukapolo. Nchifukwa chake khalidwe lake lili losasinthika, ndipo fungo lake lili lomwe lija.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mowabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wake, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; chifukwa chake makoleredwe ake alimobe mwa iye, fungo lake silinasinthika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira ubwana wake, ngati vinyo wokhazikika pa masese ake, osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina kuthira mu mtsuko wina; iye sanatengedwepo ukapolo. Nʼchifukwa chake kukoma kwake nʼkomwe kuja ndipo fungo lake silinasinthe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Moabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wace, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; cifukwa cace makoleredwe ace alimobe mwa iye, pfungo lace silinasinthika.