Jeremiah 48:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Chenjerani tsono, akubwera masiku pamene ndidzatuma anthu oti Mowabuyo adzamkhuthule ngati vinyo. Kenaka mitsuko yake itasanduka yopanda kanthu m'kati, ndidzaiphwanya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzatuma kwa iye otsanula, amene adzamtsanula iye; adzataya za mbiya zake, nadzaswa zipanda zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzatuma anthu amene amakhuthula vinyo mʼmitsuko ndipo adzamukhutula; adzakhuthula vinyo yense mitsuko yake pambuyo pake nʼkuphwanya mitsukoyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzatuma kwa iye otsanula, amene adzamtsanula iye; adzataya za mbiya zace, nadzaswa zipanda zao.