Jeremiah 48:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Woononga Mowabu ndi mizinda yake wabwera. Anyamata ake asee akupita kukaphedwa. Ikutero mfumu imene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mowabu wapasuka, akwera kulowa m'midzi yake, ndi anyamata ake osankhika atsikira kukaphedwa, ati Mfumu, dzina lake ndiye Yehova wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Owononga Mowabu ndi mizinda yake abwera ndipo ankhondo adzalowa mʼmidzi yake; anyamata ake okongola apita kukaphedwa,” ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Moabu wapasuka, akwera kulowa m'midzi yace, ndi anyamata ace osankhika atsikira kukaphedwa, ati Mfumu, dzina lace ndiye Yehova wa makamu.