Jeremiah 48:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumvereni chisoni kwambiri inu nonse anansi ake, anzake nonse amene mumamdziŵa. Ndipo munene kuti, ‘Ogo, taonani m'mene yathyokera ndodo yachifumu yamphamvu ija! Taonani m'mene yathyokera ndodo yaulemu ija!’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu nonse akumzungulira, mumchitire iye chisoni, inu nonse akudziwa dzina lake; muti, Chibonga cholimba chathyokatu, ndodo yokoma!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulireni kwambiri, inu nonse amene mwamuzungulira, inu nonse amene mumadziwa za kutchuka kwake; nenani kuti, “Taonani momwe yathyokera ndodo yamphamvu yaufumu ija, taonani momwe ndodo yaulemu yathyokera!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu nonse akumzungulira, mumcitire iye cisoni, inu nonse akudziwa dzina lace; muti, Cibonga colimba catyokatu, ndodo yokoma!