Jeremiah 48:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Inu anthu a ku Diboni, tsikanipo pa ulemerero wanu, khalani pansi poumapa. Woononga Mowabu wafika kudzamenyana nanu, wapasula malinga anu ankhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwe mwana wamkazi wokhala m'Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Mowabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsikani pa ulemerero wanu ndipo khalani pansi powuma, inu anthu okhala ku Diboni, pakuti wowononga Mowabu wabwera kudzamenyana nanu, wasakaza mizinda yanu yotetezedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwe mwana wamkazi wokhala m'Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Moabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako.