Jeremiah 48:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mowabu sakutchukanso. Adampanganirana zachiwembu ku Hesiboni, adati, ‘Tiyeni timuwononge, asakhalenso mtundu wa anthu.’ Ndipo inu okhala ku Madimeni, adzakukhalitsani chete, adzakupirikitsani ndi lupanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Palibenso kutamanda Mowabu; m'Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu wa anthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palibenso amene akutamanda Mowabu; ku Hesiboni anthu anamupanganira zoyipa: ‘Bwerani, tiyeni timuwonongeretu kuti asakhalenso mtundu wa anthu.’ Inunso anthu a ku Madimena, adzakukhalitsani chete; ankhondo adzakupirikitsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Palibenso kutamanda Moabu; m'Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu waanthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe.