Jeremiah 48:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo adzayankha kuti, ‘Ukutu Mowabu wagwa, amchititsa manyazi, mlireni mofuula. Mulengeze ku mtsinje wa Arinoni kuti Mowabu wasanduka bwinja.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mowabu wachitidwa manyazi, pakuti wathyoka; kuwa nulire, nunene m'Arinoni, kuti Mowabu wapasuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo adzayankha kuti, “Mowabu wachititsidwa manyazi, pakuti wasakazika. Lirani mwachisoni ndipo fuwulani! Lengezani ku mtsinje wa Arinoni kuti Mowabu wawonongedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Moabu wacitidwa manyazi, pakuti watyoka; kuwa nulire, nunene m'Arinoni, kuti Moabu wapasuka.