Jeremiah 48:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Inu okhala ku Mowabu, siyani mizinda yanu. Kapezeni pokhala pakati pa mathanthwe. Mukhale ngati nkhunda yomanga chisa kukamwa kwa phanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu okhala m'Mowabu, siyani midzi, khalani m'thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja chisanja chake pambali pakamwa pa dzenje.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu amene mumakhala ku Mowabu, siyani mizinda yanu ndi kukakhala pakati pa matanthwe. Khalani ngati nkhunda imene imamanga chisa chake pa khomo la phanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu okhala m'Moabu, siyani midzi, khalani m'thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja cisanja cace pambali pakamwa pa dzenje.