Jeremiah 48:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tamva za kunyada kwa Mowabu, ndi wonyadadi kwabasi. Ndi wodzikweza, wodzitama, wodzitukumula, ndipo ndi wa mtima wodzimva zedi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ife tamva kudzikuza kwa Mowabu, wadzikuza ndithu, kunyang'wa kwake, ndi kunyada kwake, ndi kudzitama kwake, ndi kudzikuza kwa mtima wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tamva za kunyada kwa Mowabu, kunyada kwake nʼkwakukulu. Ndi wodzitama, wonyada ndi wodzitukumula. Ali ndi mtima wodzikweza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ife tamva kudzikuza kwa Moabu, wadzikuza ndithu, kunyang'wa kwace, ndi kunyada kwace, ndi kudzitama kwace, ndi kudzikuza kwa mtima wace.