Jeremiah 48:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikulira anthu a ku Sibima kupambana m'mene ndidalirira anthu a ku Yazere. Iwe mzinda wa Sibima, uli ngati mpesa umene nthambi zake zidatambalala mpaka ku nyanja, kukafika mpaka ku Yazere. Woononga wasakaza zipatso zako zam'chilimwe, wasakaza mipesa yako yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazere, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira kunyanja ya Yazere; wakufunkha wagwera zipatso zako za mpakasa ndi mphesa zako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikukhetsa misozi chifukwa cha inu, kupambana momwe ndinalirira Yazeri. Inu anthu a ku Sibina muli ngati mipesa imene nthambi zake zatambalala mpaka ku Nyanja; zafika mpaka ku nyanja ya Yazeri. Wowononga wasakaza zipatso zake zachilimwe ndi mpesa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazeri, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira ku nyanja ya Yazeri; wakufunkha wagwera zipatso zako za mpakasa ndi mphesa zako.