Jeremiah 48:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kusangalala ndi kukondwa kwa dziko lachonde la Mowabu kwatha. Ndaletsa kuchucha kwa vinyo mopondera mphesa. Palibe amene akufuula mokondwa akamaponda mphesa. Kufuula kulipo, koma si kufuula kokondwa ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kusekera ndi kukondwa kwachotsedwa, kumunda wobala ndi kudziko la Mowabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kufuula; kufuula sikudzakhala kufuula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chimwemwe ndi chisangalalo zatha ku minda ya zipatso ya ku Mowabu. Ndaletsa kuchucha kwa vinyo mopsinyira mphesa; palibe amene akufuwula mokondwa akamapsinya mphesa. Ngakhale kufuwula kulipo, koma sikufuwula kwa chimwemwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kusekera ndi kukondwa kwacotsedwa, ku munda wobala ndi ku dziko la Moabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kupfuula; kupfuula sikudzakhala kupfuula.