Jeremiah 48:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nchifukwa chake mtima wanga ukulira Mowabu ngati chitoliro. Mtima wanga ukulira anthu a ku Kiriheresi ngati chitoliro, chifukwa chuma chao chonse chimene adaachipata chatheratu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake mtima wanga umlirira Mowabu monga zitoliro, ndipo mtima wanga uwalirira anthu a Kiriheresi monga zitoliro, chifukwa chake zakuchuluka zake adadzionera zatayika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nʼchifukwa chake mtima wanga ukulirira Mowabu ngati chitoliro. Mtima wanga ukulirira anthu a ku Kiri Heresi ngati chitoliro chifukwa chuma chimene anachipata chatha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace mtima wanga umlima Moabu monga zitolilo, ndipo mtima wanga uwalirira anthu a Kireresi monga zitolilo, cifukwa cace zakucuruka zace adadzionera zatayika.