Jeremiah 48:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa madenga onse a ku Mowabu ndiponso m'miseu yake simukumvekanso kanthu kena, koma kulira kokha. Ndamtswanya Mowabu ngati chiŵiya chopanda ntchito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamwamba pa machindwi a Mowabu ndi m'miseu mwake muli kulira monsemonse; pakuti ndaswa Mowabu monga mbiya m'mene mulibe chikondwero, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa madenga onse a ku Mowabu ndiponso mʼmisewu yake anthu akungolira, pakuti ndaphwanya Mowabu ngati mtsuko wopanda ntchito,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamwamba pa macindwi a Moabu ndi m'miseu mwace muli kulira monse monse; pakuti ndaswa Moabu monga mbiya m'mene mulibe cikondwero, ati Yehova.