Jeremiah 48:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Taonani m'mene watswanyikira! Tamvani m'mene akulirira anthu ake! Taonani m'mene wakhalira chofulatira mwamanyazi! Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka, chinthu chochititsa mantha kwa anzake okhala nawo pafupi,” akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yasweka bwanji! Akuwa bwanji Mowabu! Wapotoloka bwanji ndi manyazi! Chomwecho Mowabu adzakhala choseketsa ndi choopsera onse omzungilira iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Taonani mmene waphwanyikira! Tamvani momwe akulirira! Taonani momwe Mowabu wachititsidwira manyazi. Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka, chinthu chochititsa mantha kwa onse amene amuzungulira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yasweka bwanji! Akuwa bwanji Moabu! Wapotoloka bwanji ndi manyazi! Comweco Moabu adzakhala coseketsa ndi coopsera onse omzungulira iye.