Jeremiah 48:41 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mizinda idzagwidwa, malinga adzalandidwa. Tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Mowabu idzakhala ili thithithi ndi mantha, ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Keriyoti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Mowabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mizinda idzagwidwa ndipo malinga adzalandidwa. Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Mowabu idzakhala ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Keroti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Moabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.